Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 19:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitatha izi ndinamva ngati a mau akuru khamu lalikuru m'Mwamba, liri kunena, Aleluya; cipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;

2. pakuti maweruzo ace ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wacigololo wamkuru, amene anaipsa dziko ndi cigololo cace, ndipo anabwezera cilango mwazi wa akapolo ace pa dzanja lace la mkaziyo.

3. Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wace ukwera ku nthawi za nthawi.

4. Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wacifumu, nizinena, Amen; Aleluya.

5. Ndipo mau anacokera ku mpando wacifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ace onse, akumuopa iye, ang'ono ndi akuru.

6. Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikuru, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, nizinena, Aleluya; pakuti acita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.

7. Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wace wadzikonzera.

8. Ndipo anampatsa iye abvale bafuta wonyezimira woti mbu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.

9. Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.

10. Ndipo ndinagwa pa mapazi ace kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa cinenero.

11. Ndipo ndinaona mutatseguka m'Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi iye wakumkwera wochedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nacita nkhondo molungama.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 19