pakuti maweruzo ace ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wacigololo wamkuru, amene anaipsa dziko ndi cigololo cace, ndipo anabwezera cilango mwazi wa akapolo ace pa dzanja lace la mkaziyo.