Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 18:10-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. cifukwa cakuopa cizunzo cace, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuruwo, Babulo, mudzi wolimba! pakuti m'ora limodzi cafika ciweruziro canu.

11. Ndipo ocita malonda a m'dziko adzalira nadzaucitira cifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao;

12. malonda a golidi, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wace, ndi a ngale, ndi a nsaru yabafuta, ndi a cibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya pfungo lokoma, ndi cotengera ciri conse ca minyanga ya njobvu, ndi cotengera ciri conse camtengo wa mtengo wace wapatali, ndi camkuwa ndi cacitsulo, ndi cansangalabwi;

13. ndi kinamomo ndi amomo, ndi zofukiza, ndi zodzola, ndi libano, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng'ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magareta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.

14. Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakucokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse.

15. Otsatsa izi, olemezedwa nao, adzaima patali cifukwa ca kuopa cizunzo cace, nadzalira, ndi kucita cifundo;

16. nadzanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuru wobvala bafuta ndi cibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golidi, ndi mwala wa mtengo wace, ndi ngale!

17. Pakuti m'ora limodzi casanduka bwinja cuma cacikuru cotere. Ndipo watsigiro ali yense, ndi yense wakupita panyanja pakuti pakuti, ndi amarinyero, ndi onse amene amacita kunyanja, anaima patali,

18. napfuula poona utsi wa kutentha kwace, nanena, Mudzi uti ufanana ndi mudzi waukuruwo?

19. Ndipo anathira pfumbi pamitu pao, napfuula, ndi kulira, ndi kucita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuruwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, cifukwa ca kulemera kwace, pakuti m'ora limodzi unasanduka bwinja.

20. Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; cifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.

21. Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala, ngati mphero yaikuru, naiponya m'nyanja, nanena, Cotero Babulo, mudzi waukuru, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 18