Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 16:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo wacisanu ndi cimodzi anatsanulira mbale yace pa mtsinje waukuru Firate; ndi madzi ace anaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu ocokera poturuka dzuwa.

13. Ndipo ndinaona moturuka m'kamwa mwa cinjoka, ndi m'kamwa mwa cirombo, ndi m'kamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati acule;

14. pakuti ali mizimu ya ziwanda zakucita zizindikilo; zimene zituruka kumka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira ku nkhondo ya tsiku lalikuru la Mulungu, Wamphamvuyonse.

15. (Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zobvala zace, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wace.)

16. Ndipo anawasonkhanitsira ku malo ochedwa m'Cihebri Harmagedo.

17. Ndipo wacisanu ndi ciwiri anatsanulira mbale yace mumlengalenga; ndipo m'Kacisimo mudaturuka mau akuru, ocokera ku mpando wacifumu ndi kunena, Cacitika;

18. ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali 1 cibvomezi cacikuru cotero sicinaoneke ciyambire anthu padziko, cibvomezi colimba cotero, cacikuru cotero.

19. Ndipo 2 cimudzi cacikuruco cidagawika patatu, ndi midzi ya amitundu inagwa; ndipo 3 Babulo waukuru unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse cikho ca vinyo wamkali wa mkwiyo wace.

20. Ndipo 4 zisumbu zonse zidathawa, ndi mapiri sanapezeka.

21. Ndipo 5 anatsika kumwamba matalala akuru, lonse lolemera ngati talenti, nagwa pa anthu; ndipo anthu 6 anacitira Mulungu mwano cifukwa ca mliri wa matalala, pakuti m1iri wace nm waukuru ndithu.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 16