Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 12:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo cinaponyedwa pansi cinjoka cacikuru, njoka yokalambayo, iye wochedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; cinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ace anaponyedwa naye pamodzi.

10. Ndipo ndinamva mau akuru m'Mwamba, nanena, Tsopano zafika cipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wace; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.

11. Ndipo iwo anamlaka iye cifukwa ca mwazi wa Mwanawankhosa, ndi cifukwa ca mau a umboni wao; ndipo sanakonda moyo wao kungakhale kufikira imfa.

12. Cifukwa cace, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, cifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukuru, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.

13. Ndipo pamene cinjoka cinaonakuticinaponyedwa pansikudziko, cinazunza mkazi amene adabala mwana wamwamuna.

14. Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a ciombankhanga cacikuru, kuti akaulukire kucipululu, ku mbuto yace, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.

15. Ndipo inalabvulira m'kamwa mwace, potsata mkazi, madzi ngati mtsinje, kuti akakokoleredwe mkazi nao.

16. Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m'kamwa mwace, nilinameza madzi a mtsinje amene cinjoka cinalabvula m'kamwamwace.

17. Ndipo cinjoka cinakwiya ndi mkazi, nicinacoka kunka kucita nkhondondi otsala ambeu yace, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 12