Ndipo ndinamva mau akuru m'Mwamba, nanena, Tsopano zafika cipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wace; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.