Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 11:16-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo akulu makumi awiri mphambu anai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yacifumu yao, anagwa nkhope yao pansi nalambira Mulungu,

17. nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikuru, ndipo mwacita ufumu.

18. Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akuru; ndi kuononga iwo akuononga dziko.

19. Ndipo anatsegulidwa Kacisi wa Mulungu amene ali m'Mwamba; ndipo linaoneka likasa la cipangano cace, m'Kacisi mwace, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi cibvomezi, ndi matalala akuru.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 11