Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 4:10-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Tsono cinawerengedwa bwanji? m'mene iye anali wodulidwa kapena wosadulidwa? Si wodulidwa ai, koma wosadulidwa;

11. ndipo iye analandira cizindikilo ca mdulidwe, ndico cosindikiza cilungamo ca cikhulupiriro, comwe iye anali naco asanadulidwe; kuti kotero iye akhale kholo la onse akukhulupira, angakhale iwo sanadulidwa, kuti cilungamo ciwerengedwe kwa iwonso;

12. ndiponso kholo la mdulidwe wa iwo amene siali a mdulidwe okha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe a cikhulupiriro cija ca kholo lathu Abrahamu, cimene iye anali naco asanadulidwe.

13. Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowanyumba wa dziko lapansi silinapatsidwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yace mwa Lamulo, koma mwa cilungamo ca cikhulupiriro.

14. Pakuti ngati iwo a lamulo akhala olowa nyumba, pamenepo cikhulupiriro eayesedwa cabe, ndimo lonjezo layesedwa lopanda pace;

15. pakuti cilamulo cicitira mkwiyo; koma pamene palibe lamulo, pamenepo palibe kulakwa.

16. Cifukwa cace cilungamo cicokera m'cikhulupiriro, kuti cikhale monga mwa cisomo; kuti lonjezo likhale Iokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a cilamulo okha okha, komakwa iwonso a cikhulupiriro ca Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse;

17. monga kwalembedwa: Ndinakukhazika iwe kholo la mitundu yambiri ya anthu pamaso pa Mulungu amene iye anamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndi kuitana zinthu zoti palibe, monga ngati ziripo,

18. Amene anakhulupira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa conenedwaci, Mbeu yakoidzakhala yotere,

19. Ndipo iye osafoka m'cikhulupiriro sanalabadira thupi lace, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso;

20. ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeka cifukwa ca kusakhulupirira, koma analimbika m'cikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu,

21. nakhazikikanso mumtima kuti, o cimene iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakucicita.

Werengani mutu wathunthu Aroma 4