Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 13:2-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri naco cikhulupiriro conse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe cikondi, ndiri cabe.

3. Ndipo ndingakhale ndipereka cuma cangaconsekudyetsa osauka, ndipo ndingakhalendipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndiribe cikondi, sindipindula kanthu ai.

4. Cikondi cikhala cilezere, ciri cokoma mtima; cikondi sicidukidwa; cikondi sicidziwa kudzitamanda, sicidzikuza,

5. sicicita zosayenera, sicitsata za mwini yekha, sicipsa mtima, sicilingirira zoipa;

6. sicikondwera ndi cinyengo, koma cikondwera ndi coonadi;

7. cikwirira zinthu zonse, cfkhulupirira zinthu zonse, ciyembekeza zinthu zonse, cipirira zinthu zonse.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 13