Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Kuposa kwa Cikondi

1. Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe cikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.

2. Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri naco cikhulupiriro conse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe cikondi, ndiri cabe.

3. Ndipo ndingakhale ndipereka cuma cangaconsekudyetsa osauka, ndipo ndingakhalendipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndiribe cikondi, sindipindula kanthu ai.

4. Cikondi cikhala cilezere, ciri cokoma mtima; cikondi sicidukidwa; cikondi sicidziwa kudzitamanda, sicidzikuza,

5. sicicita zosayenera, sicitsata za mwini yekha, sicipsa mtima, sicilingirira zoipa;

6. sicikondwera ndi cinyengo, koma cikondwera ndi coonadi;

7. cikwirira zinthu zonse, cfkhulupirira zinthu zonse, ciyembekeza zinthu zonse, cipirira zinthu zonse.

8. Cikondi sicitha nthawizonse, koma kapena zonenera zidzakhala cabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala cabe.

9. Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.

10. Koma pamene cangwiro cafika, tsono camderamdera cidzakhalacabe.

11. Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa cabe zacibwana.

12. Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati cimbuuzi; koma R pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.

13. Ndipo tsopano zitsala cikhulupiriro, dyembekezo, cikondi, zitatu izi; koma cacikuru ca izi ndico cikondi.