Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 8:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ace ndi mudzi wace ndi dziko lace;

2. ndipo uzimcitira Ai ndi mfumu yace monga umo unamcitira Yeriko ndi mfumu yace; koma zofunkha zace ndi ng'ombe zace mudzifunkhire nokha; udziikire anthu aja lire kukhonde kwa mudzi.

3. Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,

4. nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mudzi; musakhalira kutali ndi mudzi, koma mukhale okonzekeratu nonse;

5. ndipo ine, ndi anthu onse ali nane, tidzayandikira mudzi; ndipo kudzali, pamene aturuka kudzakomana nafe, monga poyamba paja, tidzathawa pamaso pao;

6. ndipo adzaturuka kutitsata mpaka tidawakokera asiyane ndi mudzi; pakuti adzanena, Atithawa pamaso pathu monga poyamba pala; nafenso tidzathawa pamaso pao;

7. pamenepo muziuka m'molalira ndi kulowa m'mudzi; pakuti Yehova Mulungu wanu adzaupereka m'manja mwanu.

8. Ndipo kudzali, mutagwira mudzi, muzitentha mudziwo ndi moto; muzicita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani.

9. Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m'molalira, nakhala pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.

10. Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayesa anthu, nakwera, iye ndi akuru a Israyeli, pamaso pa anthu a ku Ai.

11. Ndi anthu onse a nkhondo okhala naye anakwera, nayandikira nafika pamaso pa mudzi, namanga misasa kumpoto kwa Ai; koma pakati pa iye ndi Ai panali cigwa.

12. Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m'molalira pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa mudzi.

13. Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mudzi, ndi olalira ao kumadzulo kwa mudzi, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa cigwa,

14. Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anaciona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, naturuka amuna a m'mudzi kuthirana ndi Israyeli, iye ndi anthu ace onse, poikidwiratu patsogolo pa cidikha; popeza sanadziwa kuti amlalira kukhonde kwa mudzi.

15. Ndipo Yoswa ndi Aisrayeli onse anaoneka ngati a ku Ai alikuwathyola, nathawira njira ya kucipululu.

16. Pamenepo anthu onse okhala m'mudzi, anaitanidwa awapitikitse, nampitikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mudzi.

17. Ndipo sanatsala mwamuna mmodzi yense m'Ai kapena m'Beteli osaturukira kwa Israyeli; nasiya mudzi wapululu, napitikitsa Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 8