Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 7:6-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Yoswa anang'amba zobvala zace, nagwa nkhope yace pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akulu akulu a Israyeli, nathira pfumbi pamitu pao.

7. Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordano, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordano!

8. Ndidzanenanji, Ambuye, Israyeli atabwerera m'mbuyo pamaso pa adani ao?

9. Akadzamva ici Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu pa dziko lapansi; ndipo mudzacitiranji dzina lanu lalikuru?

10. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako cotere?

11. Israyeli wacimwa, nalakwiranso cipangano canga, ndinawalamuliraco; natengakonso coperekedwaco; anabanso, nanyenganso, naciika pakati pa akatundu ao.

12. Mwa ici ana a Israyeli sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga coperekedwaco, kucicotsa pakati pa inu.

13. Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Pali coperekedwa cionongeke pakati pako, Israyeli iwe; sukhoza kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutacotsa coperekedwaco pakati panu.

14. Koma m'mawa adzakuyandikitsani, pfuko ndi pfuko; ndipo kudzali kuti pfukoli Yehova aliulula lidzayandikira mwa zibale zace; ndi cibale Yehova aciulula cidzayandikira monga mwa a nyumba ace; ndi a m'nyumbawo Yehova awaulula adzayandikira mmodzi mmodzi.

15. Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali naco coperekedwaco adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo cifukwa analakwira cipangano ca Yehova, ndi cifukwa anacita copusa m'Israyeli.

16. Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayandikizitsa Israyeli, pfuko ndi pfuko; ndi pfuko la Yuda linagwidwa;

17. nayandikizitsa zibale za Yuda, nagwira cibale ca Azari; nayandikizitsa cibale ca Azari, mmodzi mmodzi, nagwidwa Zabidi;

18. nayandikizitsa a m'nyumba yace mmodzi mmodzi; ndipo Akani, mwana wa Karimu, mwanu wa Zabidi, mwana wa Zera, wa pfuko la Yuda anagwidwa.

19. Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, ucitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israyeli, numlemekeze iye; nundiuze tsopano, wacitanji? usandibisire.

20. Ndipo Akani anayankha Yoswa nati, Zoonadi, ndacimwira Yehova Mulungu wa Israyeli, ndacita zakuti zakuti;

21. pamene ndinaona pazofunkha maraya abwino a ku Babulo, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi cikute cagolidi, kulemera kwace masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pacepo.

22. Pamenepo Yoswa anatuma mithenga, iwo nathamangira kuhema; ndipo taonani, zidabisika m'hema mwace ndi siliva pansi pace.

23. Ndipo anazicotsa pakati pa hema, nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa ana onse a Israyeli, nazitula pamaso pa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 7