Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 3:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la cipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la cipangano, natsogolera anthu.

7. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisrayeli onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.

8. Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la cipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordano muziima m'Yordano.

9. Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israyeli, Idzani kuno, mumve mau a Yehova Molungu wanu.

10. Nati Yoswa, Ndi ici mudzadziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati pa inu, ndi kuti adzapitikitsa ndithu pamaso panu Akanani, ndi Ahiti, ndi Ahivi, ndi Aperizi, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Ayebusi.

11. Taonani, likasa la cipangano La Ambuye wa dziko lonse lapansi lioloka Yordano pamaso panu,

12. Ndipo tsono, mudzitengere amuna khumi ndi awiri mwa mapfuko a Israyeli, pfuko limodzi mwamuna mmodzi.

13. Ndipo kudzakhala, akaima mapazi a ansembe akusenza likasa la Yehova Ambuye wa dziko lonse, m'madzi a Yordano, adzadulidwa madziwo, ndiwo madzi ocokera kumagwero, nadzaima mulu umodzi.

14. Ndipo kunali pocoka anthu ku mahema ao kukaoloka Yordano, ansembe anasenza likasa la cipangano pamaso pa anthu.

15. Ndipo pamene iwo akusenza likasa anafika ku Yordano, nathibika m'mphepete mwa madzi mapazi a ansembe akusenza likasa, pakuti Yordano asefuka m'magombe ace onse, nyengo yonse ya masika,

16. pamenepo madzi ocokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adamu, ndiwo mudzi wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kumka ku nyanja ya cidikha, ndiyo Nyanja ya Mcere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 3