Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 24:5-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aigupto, monga ndinacita pakati pace; ndipo nditatero ndinakuturutsani.

6. Ndipo ndinaturutsa atate anu m'Aigupto; ndipo munadzakunyanja; koma Aaigupto analondola atate anu ndi magareta ndi apakavalo mpaka ku Nyanja Yofiira.

7. Ndipo pamene anapfuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aaigupto nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya cocita Ine m'Aigupto; ndipo munakhala m'cipululu masiku ambiri.

8. Pamenepo ndinakulowetsani inu m'dziko la Aamori okhala tsidya lija la Yordano; nagwirana nanu iwowa; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu, nimunalandira dziko lao likhale lanu lanu; ndipo ndinawaononga pamaso panu.

9. Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Moabu, anauka naponyana ndi Israyeli; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu;

10. koma sindinafuna kumvera Balamu, potero anakudalitsani cidalitsire, ndipo ndinakulanelitsani m'dzanja lace.

11. Pamenepo munaoloka Yordano, ndi kufika ku Yeriko; ndi eni ace a ku Yeriko anaponyana nanu nkhondo, Aamori, ndi Aperizi, ndi Akanani, ndi Ahiti, ndi Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu.

12. Ndipo ndinatuma mabvu atsogolere inu, amene anawaingitsa pamaso panu, ndiwo mafumu awiri a Aamori; osati ndi lupanga lako, kapena ndi uta wako ai.

13. Ndipo ndinakupatsani dziko limene simunagwiramo nchito, ndi midzi simunaimanga, ndipo mukhala m'mwemo; mukudya za m'minda yamphesa, ndi minda yaazitona imene simunaioka.

14. Ndipo tsopano, opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimucotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi m'Aigupto; nimutumikire Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 24