Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 24:14-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo tsopano, opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimucotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi m'Aigupto; nimutumikire Yehova.

15. Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.

16. Ndipo anthu anayankha, nati, Sikungatheke kuti timsiye Yehova, ndi kutumikira milungu yina;

17. pakuti Yehova Mulungu wathu ndi iye amene anatikweza kutiturutsa m'dziko la Aigupto ku nyumba ya akapolo, nacita zodabwiza zazikuruzo pamaso pathu, natisunga m'njira monse tidayendamo, ndi pakati pa anthu onse amene tinapita pakati pao;

18. ndipo Yehova anaingitsa pamaso pathu anthu awa onse, ngakhale Aamori okhala m'dzikomo; cifukwa cace ifenso tidzatumikira Yehova, pakuti ndiye Mulungu wathu.

19. Ndipo Yoswa anati kwa anthu, Simukhoza inu kutumikira Yehova pakuti ndiye Mulungu woyera, ndi Mulungu wansanje; sadzalekerera zolakwa zanu, kapena zocimwa zanu.

20. Mukasiya Yehova, ndi kutumikira milungu yacilendo, adzatembenuka ndi kukucitirani coipa, ndi kukuthani, angakhale anakucitirani cokoma.

21. Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Iaitu, koma tidzatumikira Yehova.

22. Ndipo Yoswa ananena ndi anthu, Inu mwadzicitira mboni inu nokha kuti mwadzisankhira Yehova kumtumikira iye. Ndipo anati, Ndife mboni.

23. Ndipo tsopano, cotsani milungu yacilendo iri pakati pa inu, ndi kulozetsa mitima yanu kwa Yehova, Mulungu wa Israyeli.

24. Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Tidzamtumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mau ace.

25. Motero Yoswa anacita pangano ndi anthu tsiku lija, nawaikira lemba ndi ciweruzo m'Sekemu.

26. Ndipo Yoswa analembera mau awa m'buku la cilamulo ca Mulungu; natenga mwala waukuru, nauimitsa apo patsinde pa thundu wokhala pa malo opatulika a Yehova.

27. Ndipo Yoswa anati kwa anthu onse, Taonani, mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa; pakuti udamva mau onse a Yehova amene ananena kwa ife; ndipo udzakhala mboni yotsutsa inu, mungakanize Mulungu wanu.

28. Pamenepo Yoswa anauza anthu amuke, yense ku colowa cace.

29. Ndipo kunali, zitatha izi, Yoswa mwana wa Nuni mtumiki wa Yehova, adafa, wa zaka zana ndi khumi.

30. Ndipo anamuika m'malire a colowa cace m'Timinati-sera, ndiwo ku mapiri a Efraimu kumpoto kwa phiri la Gaasi.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 24