Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 23:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Potero mudzisamalire ndithu kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.

12. Koma, mukadzabwereram'mbuyo pang'ono pokha ndi kuumirira otsala a mitundu awa, ndiwo akutsala pakati pa inu, ndi kukwatitsana nao, ndi kulowana nao, naonso kulowana nanu;

13. dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwacotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.

14. Ndipo taonani, lero lino ndirikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mau amodzi; onse anacitikira inu, sanasowapo mau amodzi.

15. Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukucotsani m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.

16. Mukalakwira cipangano ca Yehova Mulungu wanu cimene analamulira inu ndi kumuka ndi kutumikira milungu yina ndi kuigwadira, mkwiyo wa Mulungu udzayakira inu, nimudzatayika msanga m'dziko lokomali anakupatsani.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 23