Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 22:2-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. nanena nao, Mwasunga inu zonsezo anakulamulirani Mosemtumiki wa Yehova; mwamveranso mau anga m'zonse ndinakulamulirani inu;

3. simunasiya abale anu masiku awa ambiri mpaka lero lino, koma mwasunga cisungire lamulola Yehova Mulungu wanu.

4. Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mu kani ku mahema anu, ku dziko la colowa canu cimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordano.

5. Koma samalirani bwino kuti mucite cilangizo ndi cilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace zonse ndi kusunga malamulo ace, ndi kumuumirira iye, ndi kumtumikira iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

6. Momwemo Yoswa anawadalitsa, nawauza amuke; ndipo anamuka ku mahema ao.

7. Ndipo gawo limodzi la pfuko la Manase, Mose anawapatsa colowa m'Basana; koma gawo lina Yoswa anawaninkha colowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordano kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa;

8. nanena nao ndi kuti, Bwererani naco cuma cambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndi siliva, ndi golidi, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi maraya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu.

9. Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anabwerera, nacoka kwa ana a Israyeli ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kumka ku dziko la Gileadi, ku dziko lao lao, limene anakhala eni ace, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 22