Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 18:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israyeli unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko cihema cokomanako; ndipo dziko linawagoniera.

2. Ndipo anatsala mwa ana a Israyeli mapfuko asanu ndi awiri osawagawira colowa cao.

3. Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israyeli, Mucedwa mpaka liti kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani?

4. Mudzifunire amuna, pfuko liri lonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati pa dziko, nalilembe monga mwa colowa cao; nabwereoso kwa ine.

5. Ndipo adzaligawa magawo asanu ndi awiri; Yuda adzakhala m'malire ace kumwela, ndi a m'nyumba ya Yosefe adzakhala m'malire mwao kumpoto.

6. Ndipo muzilemba dziko likhale magawo asanu ndi awiri, ndi kubwera nao kuno kwa ine malembo ace; ndipo ndidzakuloterani maere pane pamaso pa Yehova Mulungu wathu.

7. Pakuti Alevi alibe gawo pakati pa inu; pakuti unsembe wa Yehova ndiwo colowa cao. Koma Gadi, ndi Rubeni, ndi pfuko la Manase logawika pakati adalandira colowa cao tsidya lija la Yordano kum'mawa, cimene Mose mtumiki wa Yehova adawapatsa.

8. Ndipo amunawo ananyamuka, namuka; ndipo Yoswa analamulira opita kulemba dzikowo, ndi kuti, Mukani, muyendeyende pakati pa dziko, ndi kulilemba, oimubwerenso kwa ine, ndipo ndidzakuloterani maere pane pamaso pa Yehova pa Silo.

9. Namuka amunawo, napitapita pakati pa dziko, nalilemba m'buku, nayesa midzi yace, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku cigono ku Silo.

10. Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israyeli dziko, monga mwa magawo ao.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 18