Ndipo amunawo ananyamuka, namuka; ndipo Yoswa analamulira opita kulemba dzikowo, ndi kuti, Mukani, muyendeyende pakati pa dziko, ndi kulilemba, oimubwerenso kwa ine, ndipo ndidzakuloterani maere pane pamaso pa Yehova pa Silo.