Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 17:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Koma Tselofekadi, mwana wa Hefere, mwana wa Gileadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana amuna koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana ace akazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

4. Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazare wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse colowa pakati pa abale athu; cifukwa cace anawapatsa monga mwa lamulo La Yehova, colowa pakati pa abale a atate wao.

5. Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Gileadi ndi Basana lokhala tsidya lija la Yordano:

6. popeza ana akazi a Manase adalandira colowa pakati pa ana ace amuna; ndi dziko la Gileadi linakhala la ana a Manase otsala.

7. Ndipo malire a Manase anayambira ku Aseri, kumka ku Mika-metatu, wokhala cakuno ca Sekemu; namuka malire ku dzanja lamanja kwa nzika za Enitapua.

8. Dziko la Tapua linali la Manase; koma Tapua mpaka malire a Manase linakhala la ana a Efraimu.

9. Natsikira malire ku mtsinje wa Kana, kumwera kwa mtsinje; midzi iyi inakhala ya Efraimu pakati pa midzi ya Manase; ndi malire a Manase anali kumpoto kwa mtsinje; ndimaturukiro ace anali kunyanja;

10. kumwera nkwa Efraimu ndi kumpoto nkwa Manase, ndi malire ace ndi nyanja; ndi kumpoto anakomana ndi Aseri, ndi kum'mawa anakomana ndi Isakara.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 17