Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazare wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse colowa pakati pa abale athu; cifukwa cace anawapatsa monga mwa lamulo La Yehova, colowa pakati pa abale a atate wao.