Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 14:9-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo Mose analumbira tsiku lomwelo ndi kuti, Zedi, dzikoli phazi lako lapondapo lidzakhala colowa cako, ndi ca ana ako kosalekeza, cifukwa unatsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.

10. Ndipo tsopano, taonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi mak umi anai ndi zisanu kuyambira nthawi ija Yehova ananena kwa Mose mau awa, poyenda Israyeli m'cipululu; ndipo tsopano taonani, ndine wa zaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lero lino.

11. Koma lero lino ndiri wamphamvu monga tsiku lija anandituma Mose; monga mphamvu yanga pamene paja, momwemo mphamvu yanga tsopano, kugwira nkhondo, ndi kuturuka ndi kulowa.

12. Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi midzi yaikuru ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova.

13. Pamenepo Yoswa anamdalitsa, napatsa Kalebe mwana wa Yefune Hebroni likhale colowa cace.

14. Cifukwa cace Hebroni likhala colowa cace ca Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi mpaka lero lino; popeza anatsata Yehova Mulungu wa Israyeli ndi mtima wonse.

15. Koma kale dzina la Hebroni linali mudzi wa Ariba, ndiye munthu wamkuru pakati pa Aanaki. Ndipo dziko linapumula nkhondo.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 14