Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 11:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pamene Yabini mfumu ya ku Hazoro anacimva, anatwna kwa Yabobu mfumu ya ku Madoni, ndi kwa mfumu ya ku Simironi, ndi kwa mfumu ya ku Akasafu,

2. ndi kwa mafwnu akukhala kumpoto kumapiri, ndi kucigwa kwumwela kwa Kineroto, ndi kucidikha, ndi ku mitunda ya Doro kwnadzulo;

3. kwa Akanani kwn'mawa ndi kumadzulo, ndi kwa Aamori ndi Ahiti, ndi Aperizi ndi Ayebusi kumapiri, ndi kwa Ahivi kunsi kwa Herimoni, m'dziko la Mizipa.

4. Ndipo anaturuka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kucuruka kwao ngati mcenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magareta ambirimbiri.

5. Ndipo mafwnu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israyeli nkhondo.

6. Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope cifukwa ca iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israyeli; uziwadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agareta ao ndi moto.

7. Ndipo Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo naye, anawadzera modzidzimutsa ku madzi a Meromu, nawagwera.

8. Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israyeli, ndipo anawakantha, nawapitikitsa mpaka ku Zidoni waukulu, ndi ku MiseripotuMaimu, ndi ku cigwa ca Mizepe kum'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyira ndi mmodzi yense.

9. Ndipo Yoswa anawacitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magareta ao ndi moto.

10. Ndipo Yoswa anabwerera m'mbuyo nthawi imeneyi nalanda Hazori nakantha mfumu yace ndi lupanga; pakuti kale Hazori unali waukuru wa maufumu aja onse.

11. Ndipo anakantha amoyo onse anali m'mwemo, ndi lupanga lakuthwa, ndi kuwaononga konse, osasiyapo ndi mmodzi yense wakupuma mpweya; ndipo anatentha Hazori ndi moto.

12. Ndipo Yoswa analanda midzi yonse ya mafumu awa, ndi mafumu ao omwe nawakantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse; monga Mose mtumiki wa Yehova adalamulira.

13. Koma midzi yonse yomangidwa pa zitunda zao Israyeli sanaitentha, koma wa Hazori wokha; wnenewu Yoswa anautentha.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 11