Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 66:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti Ine ndidziwa nchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga.

19. Ndipo ndidzaika cizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisi, kwa Puli ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubali ndi Yavana, ku zisumbu zakutari, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.

20. Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magareta, ndi m'macila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamila, kudza ku phiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israyeli abwera nazo nsembe zao m'cotengera cokonzeka ku nyumba ya Yehova.

21. Ndipo ena a iwo ndidzawatenga akhale ansembe ndi Alevi, ati Yehova.

22. Pakuti monga m'mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano limene ndidzalenga, lidzakhalabe pamaso pa Ine, ati Yehova, momwemo adzakhalabe ana anu ndi dzina lanu.

23. Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzace, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira ku linzace, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova.

24. Ndipo iwo adzaturuka ndi kuyang'ana mitembo ya anthu amene andilakwira Ine, pakuti mbozi yao sidzafa, pena moto wao sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 66