Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 65:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munacita coipa m'maso mwanga, ndi kusankha cimene Ine sindinakondwera naco.

13. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi;

14. taonani, atumiki anga adzayimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wacisoni; ndipo mudzapfuula cifukwa ca kusweka mzimu.

15. Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale citemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzacha atumiki ace dzina lina;

16. comweco iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zobvuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.

17. Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwa tsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.

18. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthawi zonse ndi ici ndicilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ace okondwa.

19. Ndipo ndidzasangalala m'Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akupfuula.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 65