Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 60:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Tukula maso ako uunguze-unguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako amuna adzacokera kutari, ndi ana ako akazi adzaleredwa pambali.

5. Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, cuma ca amitundu cidzafika kwa iwe.

6. Gulu la ngamila lidzakukuta, ngamila zazing'ono za Midyani ndi Efa; iwo onsewo adzacokera ku Seba adzabwera nazo golidi ndi zonunkhira; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.

7. Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebaioti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa pa guwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.

8. Ndani awa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda ku mazenera ao?

9. Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisi kutenga ana ako amuna kutari, golidi wao ndi siliva wao pamodzi nao, cifukwa ca dzina la Yehova Mulungu wako, ndi cifukwa ca Woyera wa Israyeli, popeza Iye wakukometsa iwe.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 60