Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisi kutenga ana ako amuna kutari, golidi wao ndi siliva wao pamodzi nao, cifukwa ca dzina la Yehova Mulungu wako, ndi cifukwa ca Woyera wa Israyeli, popeza Iye wakukometsa iwe.