Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 60:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu ao adzakutumikira; pakuti m'kukwiya kwanga ndinakantha, koma mokomera mtima ndidakucitira iwe cifundo.

11. Zipata zako zidzakhalabe zotseguka, sizidzatsekedwa usana pena usiku, kuti abwere naco kwa iwe cuma ca amitundu, ndi mafumu ao otsogozedwa nao pamodzi.

12. Pakuti mtundu ndi ufumu umene udzakana kukutumikira udzaonongeka; inde mitundu imeneyo idzasakazidwa ndithu.

13. Ulemerero wa Lebano udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a kacisi wanga; ndipo ndidzacititsa malo a mapazi anga ulemerero.

14. Ndipo ana amuna a iwo amene anabvuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakucepetsa iwe adzagwadira ku mapazi ako, nadzakucha iwe, Mudzi wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israyeli.

15. Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa cangwiro cosatha, cokondweretsa ca mibadwo yambiri.

16. Iwe udzayamwanso mkaka wa amitundu, nudzayamwa bere la mafumu, nudzadziwa kuti Ine Yehova ndine mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.

17. M'malo mwa mkuwa ndidzatenga golidi, ndi m'malo mwa citsulo ndidzatenga siliva, ndi m'malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m'malo mwa miyala ndidzatenga citsulo; ndidzakuikira akapitao a mtendere, ndi oyang'anira nchito a cilungamo.

18. Ciwawa sicidzamvekanso m'dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m'malire ako; koma udzacha malinga ako Cipulumutso, ndi zipata zako Matamando.

19. Dzuwa silidzakhalanso kuunika kwako usana, ngakhale mwezi sudzakuunikiranso kuti kuyere; koma Yehova adzakhala kwa iwe kuunika kosatha, ndi Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.

20. Dzuwa lako silidzalowanso, mwezi wako sudzanka kumidima; pakuti Yehova adzakhala kuunika kwako kosatha, ndi masiku a kulira maliro ako adzatha.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 60