Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 58:5-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Kodi kusala kudya koteroko ndiko ndinakusankha? tsiku lakubvutitsa munthu moyo wace? Kodi ndiko kuweramitsa mutu wace monga bango, ndi kuyala ciguduli ndi phulusa pansi pace? Kodi uyesa kumeneko kusala kudya, ndi tsiku lobvomerezeka kwa Yehova?

6. Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga gori, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti mutyole magori onse?

7. Kodi si ndiko kupatsa cakudya cako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? pakuona wamalisece kuti umbveke, ndi kuti usadzibisire wekha a cibale cako?

8. Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kucira kwako kudzaonekera msanga msanga; ndipo cilungamo cako cidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wocinjiriza pambuyo pako.

9. Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzapfuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati ucotsa pakati pa iwe gori, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,

10. ndipo ngati upereka kwa wanjala cimene moyo Iwako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wobvutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;

11. ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'cirala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ace saphwa konse.

12. Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzachedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo.

13. Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kucita kukondwerera kwako tsiku: langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osacita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;

14. pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa colowa ca kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 58