Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 57:10-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Unatopa ndi njira yako yaitari; koma sunanene, Palibe ciyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; cifukwa cace sunalefuka.

11. Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kucita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhala cete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiopa Ine konse?

12. Ndidzaonetsa cilungamo cako ndi nchito zako sudzapindula nazo.

13. Pamene pakupfuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzacotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala naco colowa m'phiri langa lopatulika.

14. Ndipo adzanena, Undani, undani, konzani njira, cotsani cokhumudwitsa m'njira mwa anthu anga.

15. Pakuti atero Iye amene ali wamtari wotukulidwa, amene akhala mwacikhalire, amene dzina lace ndiye Woyera, Ndikhala m'malo atari ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzicepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzicepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.

16. Pakuti sindidzatsutsana ku nthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.

17. Cifukwa ca kuipa kwa kusirira kwace ndinakwiya ndi kummenya iye; ndinabisa nkhope yanga, ndipo ndinakwiya; ndipo iye anankabe mokhota m'njira ya mtima wace.

18. Ndaona njira zace, ndipo ndidzamciritsa; ndidzamtsogoleranso, ndi kumbwezera iye ndi olira maliro ace zotonthoza mtima.

19. Ndilenga cipatso ca milomo, Mtendere, mtendere kwa iye amene ali kutari, ndi kwa iye amene ali cifupi, ati Yehova; ndipo ndidzamciritsa iye.

20. Koma oipa ali ofanana ndi nyanja yowinduka; pakuti siingapume, ndi madzi ace autsa matope ndi ubve.

21. Palibe mtendere, ati Mulungu wanga, kwa oipa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 57