Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 55:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndarama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndarama ndi opanda mtengo wace.

2. Bwanji inu mulikutayira ndarama cinthu cosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye cimene ciri cabwino, moyo wanu nubondwere ndi zonona.

3. Cherani Lhutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu cipangano cosatha, ndico zifundo zoona za Davide.

4. Taonani, ndampereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.

5. Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwa, ndi mtundu umene sunakudziwa udzakuthamangira, cifukwa ca Yehova Mulungu wako, ndi cifukwa ca Woyera wa Israyeli; pakuti Iye wakukometsa.

6. Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi;

7. woipa asiye njira yace, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ace, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamcitira cifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.

8. Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu siziri njira zanga, ati Yehova.

9. Pakuti monga kumwamba kuli kutari ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga ziri zazitari kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.

10. Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kucokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzyala, ndi cakudya kwa wakudya;

11. momwemo adzakhala mau anga amene aturuka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine cabe, koma adzacita cimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 55