Bwanji inu mulikutayira ndarama cinthu cosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye cimene ciri cabwino, moyo wanu nubondwere ndi zonona.