Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 52:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Cifukwa cace kodi ndicitenji pano? ati Yehova; popeza anthu anga acotsedwa popanda kanthu? akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa licitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.

6. Cifukwa cace anthu anga adzadziwa dzina langa; cifukwa cacersiku limenelo iwo adzadziwa kuti Ine ndine amene ndinena; taonani, ndine pano.

7. Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa cipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.

8. Mau a alonda ako! akweza mau, ayimba pamodzi; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Yehova abwerera kudza ku Ziyoni.

9. Kondwani zolimba, yimbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ace, waombola Yerusalemu.

10. Yehova wabvula mkono wace woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona cipulumutso ca Mulungu wathu.

11. Cokani inu, cokani inu, turukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; turukani pakati pace, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.

12. Pakuti simudzacoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israyeli adzadikira pambuyo panu.

13. Taonani, Mtumiki wanga adzacita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.

14. Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israyeli, momwemo nkhope yace yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu ali yense, ndi maonekedwe ace kupambana ana a anthu;

15. momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti cimene sicinauzidwa kwa iwo adzaciona, ndi cimene iwo sanamva adzazindikira.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 52