Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 50:3-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndibveka thambo ndi kuda, ndi kuyesa ciguduli copfunda cace.

4. Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akucirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi im'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.

5. Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.

6. Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisira nkhope yanga manyazi ndi kulabvulidwa.

7. Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; cifukwa cace sindinasokonezedwa; cifukwa cace ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi.

8. Iye ali pafupi amene alungamitsa Ine; ndani adzakangana ndi Ine? tiyeni tiimirire tonse pamodzi; mdani wanga ndani? andiyandikire.

9. Taonani, Ambuye Yehova adzathandiza Ine; ndani amene adzanditsutsa? taonani, iwo onse adzatha ngati cobvala, njenjete zidzawadya.

10. Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wace? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wace.

11. Taonani, inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzimangira m'cuuno ndi nsakali, yendani inu m'cirangati ca moto wanu, ndi pakati pa nsakali zimene mwaziyatsa. Ici mudzakhala naco ca pa dzanja langa; mudzagona pansi ndi cisoni.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 50