Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akucirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi im'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.