Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 49:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutari; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anachula dzina langa;

2. nacititsa pakamwa panga ngati lupanga lakuthwa, mu mthunzi wa dzanja lace wandibisa Ine; wandipanga Ine mubvi wotuulidwa; m'phodo mwace Iye wandisungitsa Ine, nati kwa Ine,

3. Iwe ndiwe mtumiki wanga, Israyeli, amene ndidzalemekezedwa nawe.

4. Koma ndinati, Ndagwira nchito mwacabe, ndatha mphamvu zanga pacabe, ndi mopanda pace; koma ndithu ciweruziro canga ciri ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga.

5. Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wace, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israyeli asonkhanidwe kwa Iye; cifukwa Ine ndiri wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga;

6. inde, ati, Ciri cinthu copepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israyeli; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale cipulumutso canga mpaka ku malekezero a dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 49