Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 45:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za m'menemo, ndinazilamulira ndine.

13. Ine ndautsa Koresi m'cilungamo, ndipo ndidzalungamitsa njira zace zonse; iye adzamanga mudzi wanga, nadzaleka andende anga anke mwa ufulu, wosati ndi mtengo pena mphotho, ati Yehova wa makamu.

14. Atero Yehova, Nchito ya Aigupto, ndi malonda a Kusi, ndi a Sabea, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.

15. Ndithu Inu ndinu Mulungu, amene mudzibisa nokha, Mulungu wa Israyeli, Mpulumutsi.

16. Iwo adzakhala ndi manyazi, inde, adzathedwa nzeru onsewo; adzalowa m'masokonezo pamodzi, amene apanga mafano.

17. Koma Israyeli adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi cipulumutso cosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru ku nthawi zosatha.

18. Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwacabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.

19. Ine sindinanena m'tseri m'malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwacabe; Ine Yehova ndinena cilungamo, ndinena zimene ziri zoona.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 45