Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani cifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mlungu wosakhoza kupulumutsa.