Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 45:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atero Yehova kwa wodzozedwa wace kwa Koresi, amene dzanja lace lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pace, ndipo ndidzamasula m'cuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pace, ndi zipata sizidzatsekedwa:

2. Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzatyolatyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapici acitsulo;

3. ndipo ndidzakupatsa iwe cuma ca mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israyeli.

4. Ndakuitana iwe dzina lako, cifukwa ca Yakobo mtumiki wanga ndi Israyeli wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwa Ine.

5. Ine ndiri Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'cuuno, ngakhale sunandidziwa;

6. kuti anthu akadziwe kucokera ku maturukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.

7. Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi coipa, Ine ndine Yehova wocita zinthu zonse zimenezi.

8. Igwani pansi, inu m'mwamba, kucokera kumwamba, thambo litsanulire pansi cilungamo; dziko lapansi litseguke, kuti libalitse cipulumutso, nilimeretse cilungamo cimere pamodzi; Ine Yehova ndinacilenga cimeneco.

9. Tsoka kwa iye amene akangana ndi Mlengi wace! phale mwa mapale a dziko lapansi! Kodi dongo linganene kwa iye amene aliumba, Kodi upanga ciani? pena nchito yako, Iye alibe manja?

10. Tsoka kwa iye amene ati kwa atate wace, Kodi iwe ubalanji? pena kwa mkazi, Ulikusauka ninji iwe?

11. Atero Yehova Woyera wa Israyeli ndi Mlengi wace, Ndifunse Ine za zinthu zimene zirinkudza; za ana anga amuna, ndi za nchito ya manja anga, ndilamulireni Ine.

12. Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za m'menemo, ndinazilamulira ndine.

13. Ine ndautsa Koresi m'cilungamo, ndipo ndidzalungamitsa njira zace zonse; iye adzamanga mudzi wanga, nadzaleka andende anga anke mwa ufulu, wosati ndi mtengo pena mphotho, ati Yehova wa makamu.

14. Atero Yehova, Nchito ya Aigupto, ndi malonda a Kusi, ndi a Sabea, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 45