Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 44:24-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Atero Yehova, Mombolo wako, ndi Iye amene anakuumba iwe m'mimba, Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, ndi kufunyulula ndekha zakumwamba, ndi kuyala dziko lopansi; ndani ali ndi Ine?

25. Ndine amene nditsutsa zizindikilo za matukutuku, ndi kucititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:

26. Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kucita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za midzi ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ace.

27. Ndine amene nditi kwa nyanja yakuya, Iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako;

28. ndi kunena za Koresi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzacita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kacisi, Maziko ako adzaikidwa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 44