Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 41:11-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati cabe, nadzaonongeka.

12. Iwe udzawafuna osawapeza, ngakhale iwo amene akangana ndi iwe; ocita nkhondo ndi iwe, adzakhala ngati cabe, ndi monga kanthu kopanda pace.

13. Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.

14. Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israyeli; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israyeli.

15. Taona, ndidzakuyesa iwe coombera tirigu catsopano cakuthwa cokhala ndi mano; iwe udzaomba mapiri ndi kuwapera asalale, ndi kusandutsa zitunda mungu.

16. Iwe udzawakupa, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kabvumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israyeli,

17. Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilume lao lilephera, cifukwa ca ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israyeli sindidzawasiya.

18. Ndidzagwetsa mitsinje pazitunda zoti se, ndi akasupe pakati pa zigwa; ndidzasandutsa cipululu, cikhale thamanda lamadzi, ndi mtunda wouma ukhale magwero a madzi.

19. Ndidzabzala m'cipululu mkungudza, ndi msangu, ndi mcisu, ndi mtengo waazitona; ndidzaika m'cipululu pamodzi mlombwa, ndi mkuyu, ndi naphini;

20. kuti iwo aone ndi kudziwa, ndi kulingalira, ndi kumvetsa pamodzi, kuti dzanja la Yehova lacita ici, ndipo Woyera wa Israyeli wacilenga ici.

21. Onetsani mlandu wanu, ati Yehova; turutsani zifukwa zanu zolimba, ati Mfumu ya Yakobo.

22. Aziturutse, atichulire ife, cimene cidzaoneka; chulani inu zinthu zakale, zinali zotani, kuti ife tiganizire pamenepo, ndi kudziwa mamariziro ao; kapena tionetseni ife zinthu zimene zirinkudza.

23. Chulani zinthu zimene zirinkudza m'tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, citani zabwino, kapena citani zoipa, kuti ife tiopsyedwe, ndi kuona pamodzi.

24. Taonani, inu muli acabe, ndi nchito yanu yacabe; wonyansa ali iye amene asankha inu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 41