Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 36:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ine nditi, Uphungu wako, ndi mphamvu zako za kunkhondo, zingokhala mau acabe; tsopano ukhulupirira yani, kuti wandipandukira ine?

6. Taona, ukhulupirira ndodo yabango iyi yophwanyika, kunena Aigupto; imene munthu akaitsamira, idzalowa m'dzanja mwace, ndi kulipyoza; momwemo Farao, mfumu ya Aigupto, kwa onse amene amkhulupirira iye.

7. Koma ukanena kwa ine, Ife tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; kodi si ndiye amene Hezekiya wacotsa misanje yace ndi maguwa ace a nsembe, nati kwa Yuda, ndi kwa Yerusalemu, Inu mudzapembedzera patsogolo pa suwa la nsembe ili?

8. Cifukwa cace upereketu zikole kwa mbuyanga, mfumu ya Asuri, ndipo ine ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo.

9. Bwanji tsono iwe ungathe kubweza nkhope ya nduna mmodzi wamng'ono wa atumiki a mbuyanga, ndi kukhulupirira Aigupto, kuti adzakupatsa magareta ndi apakavalo?

10. Ndipo ine tsopano, kodi ndafika opanda Yehova kudzamenyana ndi dziko ili, kudzalipasula? Yehova anati kwa ine, Kwera, ndi kumenyana ndi dziko ili, ndi kulipasula.

11. Ndipo Eliakimu, ndi Sebina, ndi Yoaki, anati kwa kazembeyo, Nenanitu kwa atumiki anu m'cinenero ca Aramu; pakuti ife ticimva; ndipo musanene kwa ife m'Ciyuda, m'makutu a anthu amene ali palinga.

12. Koma kazembeyo anati, Kodi mbuyanga ananditumiza ine kwa mbuyako ndi kwa iwe kunena mau amenewa? kodi iye sananditumiza ine kwa amuna okhala palinga, kuti adye ndowe zao zao, ndi kumwa madzi ao ao ndi inu?

13. Pamenepo kazembeyo anaima, napfuula ndi mau akuru m'Ciyuda, nati, Imvani, inu, mau a mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 36