Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 36:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma panali caka cakhumi ndi cinai ca mfumu Hezekiya, Sanakeribu, mfumu ya Asuri anadza, nathira nkhondo pa midzi ya malinga yonse ya Yuda, nailanda.

2. Ndipo mfumu ya Asuri inatumiza kazembe kucokera pa Lakisi, kunka ku Yerusalemu, kwa mfumu Hezekiya, ndi nkhondo yambiri. Ndipo iye anaima cifupi ndi mcerenje wa thamanda la kumtunda, m'khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsaru.

3. Ndipo anamturukira Eliakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yoaki, mwana wa Asafu, mkumbutsi.

4. Ndipo kazembeyo anati kwa iwo, Nenani inu tsopano kwa Hezekiya, Itero mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri, Kodi cikhulupiriro ici ncotani, ucikhulupirira iwe?

5. Ine nditi, Uphungu wako, ndi mphamvu zako za kunkhondo, zingokhala mau acabe; tsopano ukhulupirira yani, kuti wandipandukira ine?

6. Taona, ukhulupirira ndodo yabango iyi yophwanyika, kunena Aigupto; imene munthu akaitsamira, idzalowa m'dzanja mwace, ndi kulipyoza; momwemo Farao, mfumu ya Aigupto, kwa onse amene amkhulupirira iye.

7. Koma ukanena kwa ine, Ife tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; kodi si ndiye amene Hezekiya wacotsa misanje yace ndi maguwa ace a nsembe, nati kwa Yuda, ndi kwa Yerusalemu, Inu mudzapembedzera patsogolo pa suwa la nsembe ili?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 36