Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 30:22-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo mudzaipitsa cokuta ca mafano ako, osema asiliva, ndi comata ca mafano ako osungunula agolidi; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Cokani.

23. Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wace adzaca bwino ndi kucuruka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo akuru.

24. Momwemonso ng'ombe ndi ana a buru olima nthaka adzadya cakudya cocezera, cimene capetedwa ndi cokokolera ndi mkupizo.

25. Ndipo pamwamba pa mapiri akuru onse, ndipa zitunda zonse zazitaritari padzakhala mitsinje ndi micerenje ya madzi, tsiku lophana lalikuru, pamene nsanja zidzagwa.

26. Komanso kuwala kwace kwa mwezi kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa, ndi kuwala kwa dzuwa kudzakula monga madzuwa asanu ndi awiri, monga kuwala kwa masiku asanu ndi awiri, tsiku limenelo Yehova adzamanga bala la anthu ace, nadzapoletsa khana limene anawakantha ena.

27. Taonani, dzina la Yehova licokera kutari, mkwiyo wace uyaka, malawi ace ndi akuru; milomo yace iri yodzala ndi ukali, ndi lilime lace liri ngati moto wonyambita;

28. ndi mpweya wace uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m'khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi copetera ca cionongeko; ndi capakamwa calakwitsa, cidzakhala m'nsagwada za anthu.

29. Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi citoliro, kufikira ku phiri la Yehova, ku thanthwe la Israyeli,

Werengani mutu wathunthu Yesaya 30