Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 30:17-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Cikwi cimodzi cidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba pa phiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa citundu.

18. Cifukwa cace Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo cifukwa cace Iye adzakuzidwa, kuti akucitireni inu cifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa ciweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.

19. Pakuti anthu adzakhala m'Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kupfuula kwako; pakumva Iye adzayankha.

20. Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu cakudya ca nsautso, ndi madzi a cipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako;

21. ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.

22. Ndipo mudzaipitsa cokuta ca mafano ako, osema asiliva, ndi comata ca mafano ako osungunula agolidi; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Cokani.

23. Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wace adzaca bwino ndi kucuruka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo akuru.

24. Momwemonso ng'ombe ndi ana a buru olima nthaka adzadya cakudya cocezera, cimene capetedwa ndi cokokolera ndi mkupizo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 30