Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 29:6-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Yehova wa makamu adzamzonda ndi bingu, ndi cibvomezi, ndi mkokomo waukuru, kabvumvulu, ndi mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita.

7. Ndipo khamu la mitundu yonse yomenyana ndi Arieli, ngakhale yonse yomenyana naye ndi linga lace, ndi kumsautsa idzafanana ndi loto, masomphenya a usiku.

8. Ndipo kudzafanana ndi munthu wanjala, pamene alota, ndipo, taonani, akudya; koma auka, ndipo m'kati mwace muli zi; kapena monga munthu waludzu pamene alota, ndipo, taonani, akumwa; koma auka ndipo taonani walefuka, ndipo m'kati mwace muli gwa; momwemo lidzakhala khamu la mitundu yonse yomenyana ndi phiri la Ziyoni.

9. Khalani ndi kudabwa; sangalalani ndi kukhala akhungu; iwo aledzera, koma si ndi vinyo, ali dzandi dzandi; koma si ndi cakumwa caukali.

10. Pakuti Yehova watsanulira pa inu mzimu wa tulo togonetsa, natseka maso anu, ndiwo aneneri; naphimba mitu yanu, ndiwo alauli.

11. Ndipo masomphenya onse akusandukirani mau a m'buku limatidwa ndi phula, limene anthu amapereka kwa wina wodziwa kuwerenga, nati, Werengani umu; koma ati, Sindingathe, cifukwa lamatidwa ndi phula;

12. ndipo buku laperekedwa kwa wosadziwa kuwerenga, ndi kuti, Werengani umu; koma ati, Ine sindinaphunzira.

13. Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutari ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;

14. cifukwa cace, taonani, ndidzacitanso mwa anthu awa nchito yodabwitsa, ngakhale nchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika.

15. Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi nchito zao ziri mumdima, ndipo amati Ndani ationa ife? ndani atidziwa ife?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 29