Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 29:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. cifukwa cace, taonani, ndidzacitanso mwa anthu awa nchito yodabwitsa, ngakhale nchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika.

15. Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi nchito zao ziri mumdima, ndipo amati Ndani ationa ife? ndani atidziwa ife?

16. Ozolitsa inu! Kodi woumba adzayesedwa ngati dothi; kodi cinthu copangidwa cinganene za iye amene anacipanga, Iye sanandipanga ine konse; kapena kodi cinthu coumbidwa cinganene za iye amene anaciumba, Iye alibe nzeru?

17. Kodi sikatsala kamphindi kakang'ono, ndipo Lebano adzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango?

18. Ndipo tsiku limenelo gonthi adzam va mau a m'buku, ndi maso akhungu adzaona poturuka m'zoziya ndi mumdima.

19. Ofatsanso kukondwa kwao kudzacuruka mwa Yehova, ndi aumphawi a mwa anthu adzakondwerera mwa Woyera wa Israyeli.

20. Pakuti woopsya wagoma, ndi wonyoza watha, ndi onse odikira zolakwa alikhidwa;

21. amene apalamulitsa munthu mlandu, namchera msampha iye amene adzudzula pacipata, nambweza wolungama ndi cinthu cacabe.

22. Cifukwa cace Yehova amene anaombola Abrahamu, atero za banja la Yakobo: Yakobo sadzakhala ndi manyazi tsopano, ngakhale nkhope yace tsopano sidzagwa.

23. Koma pamene iye aona ana ace, nchito ya manja anga, pakati pa iye, iwo adzayeretsa dzina langa; inde, iwo adzayeretsa Woyera wa Yakobo, nadzaopa Mulungu wa Israyeli.

24. Iwonso osocera mumzimu adzadziwa luntha, ndi iwo amene ang'ung'udza adzaphunzitsidwa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 29