Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 25:8-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Iye wameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo citonzo ca anthu ace adzacicotsa pa dziko lonse lapansi; cifukwa Yehova wanena.

9. Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndikusekereram'cipulumutso cace.

10. Cifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Moabu adzaponderezedwa pansi m'malo ace, monga maudzu aponderezedwa padzala.

11. Ndipo iye adzatambasula manja ace pakati pamenepo, monga wosambira atambasula manja ace posambira; koma Iye adzagwetsa pansi kunyada kwace, pamodzi ndi kunyenga kwa manja ace.

12. Ndipo linga la pamsanje la macemba ako Iye waligwetsa, naligonetsa pansi, nalifikitsa padothi, ngakhale papfumbi.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 25