Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 24:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Taonani, Yehova apululutsa dziko, nalipasula, nalitembenuza dodolido, nabalalitsa okhalamo ace.

2. Ndipo padzakhala monga ndi anthu, moteronso ndi ansembe; monga ndi mtumiki, moteronso ndi mbuyace; monga ndi mdzakazi, moteronso ndi mbuyace wamkazi; monga ndi wogula, moteronso ndi wogulitsa; monga ndi wobwereka, moteronso ndi wombwereka; monga ndi wotenga phindu, moteronso ndi wombwezera phindu kwa iye.

3. Dziko lidzapululuka konse, ndi kupasulidwa ndithu; pakuti Yehova ananena mau amenewa.

4. Dziko lilira nilifota, dziko lilefuka nilifota, anthu omveka a padziko alefuka.

5. Dzikonso laipitsidwa ndi okhalamo ace omwe, cifukwa iwo alakwa pamalamulo nasinthanitsa malemba, natyola cipangano ca nthawi zonse.

6. Cifukwa cace citemberero cadya dziko, ndi amene akhala m'menemo apezedwa ocimwa, cifukwa cace okhalamo a padziko atenthedwa, ndipo anthu owerengeka atsala.

7. Vinyo watsopano alira, mpesa ulefuka, mitima yonse yokondwa iusa moyo.

8. Kusangalala kwa mangaka kwalekeka, phokoso la iwo amene aserera litha, kukondwa kwa mngoli kwalekeka.

9. Iwo sadzamwa vinyo ndi kuyimba nyimbo; cakumwa caukali cidzawawa kwa iwo amene acimwa.

10. Mudzi wosokonezeka wagwetsedwa pansi; nyumba zonse zatsekedwa, kuti asalowemo munthu.

11. Muli mpfuu m'makwalala cifukwa ca vinyo; kukondwa konse kwadetsedwa, kusangalala kwa dziko kwatha.

12. M'mudzi mwatsala bwinja, ndi cipata camenyedwa ndi cipasuko.

13. Cifukwa cace padzakhala cotero pakati pa dziko mwa anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo waazitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ace.

14. Amenewa adzakweza mau ao, nadzapfuula; cifukwa ca cifumu ca Yehova, iwo adzapfuula zolimba panyanja.

15. Cifukwa cace lemekezani inu Yehova kum'mawa, ngakhale dzina la Yehova, Mulungu wa Israyeli, m'zisumbu za m'nyanja.

16. Kucokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa ine! amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga.

17. Mantha ndi dzenje ndi msampha ziri pa iwe, wokhala m'dziko.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 24