Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 11:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo ng'ombe yaikazi ndi cirombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao ang'ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng'ombe.

8. Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lace m'pfunkha la mphiri.

9. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m'phiri langa lonse loyera, cifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga mdazi adzaza nyanja.

10. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Jese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pace padzakhala ulemerero.

11. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kaciwiri ndi dzanja lace anthu ace otsala ocokera ku Asuri, ndi ku Aigupto, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja yamcere.

12. Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israyeli, namema obalalika a Yuda, kucokera ku madera anai a dziko lapansi.

13. Ndipo nsanje ya Efraimu idzacoka, ndi iwo amene abvuta Yuda adzadulidwa; Efraimu sacitira nsanje Yuda, ndi Yuda sacitira nsanje Efraimu.

14. Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Moabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.

15. Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Aigupto; ndipo ndi mphepo yace yopsereza adzagwedeza dzanja lace pa Nyanja, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma.

16. Ndipo padzakhala khwalala la anthu ace otsala ocokera ku Asuri; monga lija la Israyeli tsiku lokwera iwo kuturuka m'dziko la Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 11